Kachilombo ka Korona
Matenda a korona kovidi-19 ndi matenda opatsilana oyambitsidwa ndi kachirombo ka Korona kotchedwa severe acute respiratory syndrome coronavirus 2 (SARS-CoV-2) muchingerezi. Munthu wodwala woyamba wa matendawa anapezeka mu mzinda wa Wuhan ku China mu mwezi wa Disembala mu chaka cha 2019.
Zizindikilo za matendawa ndi zosiyanasiyana, koma nthawi zambiri munthu odwala amakhala ndi listipa,kutentha thupi, kukhosomola, kutopa, kuvutika kupuma ndi kusiya mvumva fungo ndi kumva makomedwe a zinthu mkamwa. Zizindikiro zimayamba mu masiku khumi ndi anayi amene munthu anatenga kachilomboka. Anthu ambiri (81%) sadwala kwambiri (chibayo cha pang'ono), pamene 14% amadwala kwambiri, 5% amadwala mwa kayakaya (kukanika kupuma kapena ziwalo kufa)[1]. Munthu mmodzi mwa atatu aliyense sakhala ndi zizindikiro za mtendawa koma amatha kufalitsa kachilombo ka Kovidi. Odwala ena amatha kuwonetsa zizindikiro za kovidi nthawi yayitali ngakhale achila makamaka pamene ziwalo nzathupi zawonongeka. Akatswiri a Sayansi akuchitabe kafukufuka kufana kupeza zomwe zimayambita anthu kuti azikhala ndi zizindikilo za kovid nthawi yayitali.
Kachilombo ka vayilasi kamene kamayambitsa Kovidi-19 kamafalitsiwa nthawi zambiri ngati munthu amene ali ndi kachilomboka akhala pafupi ndi anthu ena. Timalovu ndi timadzi tochokela mu mphuno tikhoza kufalitsidwa ndi munthu wodwala pamene akupuma, kuyetsemula, kukhosomola, kuyimba ndi kuyankhula. Anthu ena amadwala ngati kachilombo kalowa mkamwa, mphuno kapena mmaso. Kavayilasika kamathanso kufalitsidwa ndi mmalo ogwilika monga zikupa ndi zitseko ngakhale kafukufuka akuwonetsa kuti sinjira yayikulu imene kachilomboka kakufalitsidwila [2]. Njira yakafalitsidwe kamatendawa sikakudziwika kwenikweni koma ambiri akuganiza kuti anthu akakhala kwambiri nthawi yayitali akhoza kupatsilana matenda. Munthu amene ali ndi matendawa akhoza kufalitsa kachilombo ka Kovidi masiku awiri asanayambe kuwonetsa zizindikiro, mmenenso anthu amene alibe zizindikiro angafalistilre matendawa. Anthu akhoza kufalitsa matendawa mpakana masiku khumi ngati adwala pang'ono ndipo masabata wiri (masiku khumi ndi anayi (14)) kwa amene adwala kwambiri. Njira zoyezela matendawa zosiyanasiyana zapangidwa. Njira imene ikugwiritsidwa ntchito kwambiri ndi yotchedwa real-time reverse transcription polymerase chain reaction (rRT-PCR) imene amagwiritsa tizinthu tochokera pa khosi pa munthu wodwala.
Njira zopewera matendawa ndi kupewa kuyandikilana ndi anthu, kukhala mumbindikiro, kukhala ndi mpheya mu zipinda, kuvindikila kukamwa ndi mphuno po khosomola ndi kuyetsemula, kusamba mmanja ndi kusazigwira kumaso ndi manja osasamba. Akatswlri akulangiza anthu kuvala masiki mmalo omwe kumapezeka anthu ngati m'misika. Katemera wa matendawa akupangidwa ndipo mayiko ambiri ayamba kale kubaya anthu awo.
Ngakhale ntchito ili mkati kufufuza makhwala amene angaletse kachilimboka, chisamaliro chikuperekedwa kuthana ndi zizindikiro zamatendawa basi. Monga kuchiza zizindikiro ndi makhwala, kuyika anthu odwala mmalo awokha ndi njira zina zomwe zikungoyeseledwa chabe.
Zolemba
[Sinthani | sintha gwero]- ↑ "Interim Clinical Guidance for Management of Patients with Confirmed Coronavirus Disease (COVID-19)". U.S. Centers for Disease Control and Prevention (CDC). 6 April 2020. Archived from the original on 2 March 2020. Retrieved 19 April 2020.
- ↑ "Coronavirus Disease 2019 (COVID-19)". U.S. Centers for Disease Control and Prevention (CDC). 11 February 2020. Retrieved 6 December 2020.