Prayer and Fasting Petitions Jan 2024

Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 4

MLOMBWA CCAP

ZOPEMPHERERA M’MASIKU 21 AKUPEMPHERA NDI KUSALA KUDYA


MUTU WA 2024: YENDANI MMOYO WOYENERA MAITANIDWE ANU (AEFESO 4:1)
MUTU WA MAPEMPHERO ATHU: MULUNGU WAKUITANANI NDI CHOLINGA

GAWO TSIKU ZOPEMPHERERA MAU A MULUNGU


1) Thokozani Mulungu chifukwa cha chaka
chatsopa cha 2024.
2) Mulungu watipulumutsa ku zambiri
m’chaka chapitachi, monga: ngozi,
Kuyamika Day 1 Masalmo
matenda ndi miliri.
Mulungu (02/01/2024) 136:1-26
3) Kukhazikitsa chipambano m’chaka cha
2024. Mulungu atiteteze, atisamalire,
atichize, atipambanitse komanso atidalitse
m’chaka chimenechi.
1) Vomerezani kuperewera kwanu pamaso
pa Mulungu.
2) Lapani tchimo lililonse lomwe
Day 2 mukulikumbukira ndikupempha Mulungu
Kulapa 1 Yohane 1:8-10
(03/01/2024) akukhululukireni.
3) Vomerezani magawo amene inu
(komanso mpingo) mwalephera kuchita
bwino.
1) Pemphererani banja lanu.
2) Pemphererani ntchito yanu.
Moyo
Day 3 3) Pemphererani business yanu.
wanu wa Mateyu 7:12
(04/01/2024) 4) Pemphererani sukulu yanu.
kuthupi
5) Pemphererani zina zonse zomwe inu
mumachita.
Moyo 1) Kubereka chipatso cha Mzimu Woyera. Agalatiya 5:22-23
Day 4
wanu wa 2) Kugwiritsa bwino ntchito mphatso za
(05/01/2024)
uzimu Mzimu Woyera. 1 Akorinto 12:1-11
1) Anthu azindikire kuti ayitanidwa ndi
Mulungu.
Day 5 2) Mpingo uzindikire kuti unakhazikitsidwa
2 Timoteo 1:9
(06/01/2024) ndi cholinga.
3) Mulungu ativumbulutsire chifuniro
Mutu wa chake pa miyoyo yathu.
2024 1) Mutu umenewu upindulire anthu
ochuluka.
Day 6 2) Mutu umenewu utsitsimutse miyoyo Deuteronomo
(07/01/2024) yambiri. 29:29
3) Mulungu avumbulutse zinsinsi zake
kudzera pa mutu umenewu.

Mlombwa CCAP – Evangelism Department 1 of 4


4) Mulungu agwiritse ntchito atumiki ake
modabwitsa pa mutu umenewu.
5) Pemphererani aliyense amene ataikidwe
pa program yolalikira m’chaka chimenechi.
1) Yamikani Mulungu chifukwa cha zonse
zimene zachitika mu 2023.
Day 7
2) Pemphererani atsogoleri athu onse. 1 Mbiri 28:9
(08/01/2024)
3) Pemphererani abusa athu onse.
4) Pemphererani ma komiti athu onse.
Mlombwa 1) Pemphererani ma program a 2024 kuti
CCAP Mulungu atsogolere mu zonse.
2) Pempherani kuti mpingo wathu ukhale
Day 8
chitsanzo chabwino komanso kuwala Mateyu 5:13-16
(09/01/2024)
ndinso mchere m’dera lathu.
3) Tikhale ndi kuthekera kopitiriza kufikira
ena omwe ali osowa.
* Utsogoleri wake
1) Tithokoze Mulungu chifukwa cha adindo
atsopano a Synod yathu.
Day 9
2) Mulungu awathandize kuti akwaniritse Miyambo 2:1-8
(10/01/2024)
chifuniro chake pakutsogolera Synod.
3) Mulungu awapatse nzeru komanso
Mzimu wachidziwitso.
* Moyo wa uzimu
1) Pemphererani chitsitsimutso mu Synod
Day 10 yathu. Machitidwe
(11/01/2024) 2) Pempherani kuti uthenga wabwino wa 3:19-21
chipulumutso ulalikidwe ponse-ponse.
3) Pemphererani umodzi pakati pa abusa.
* Nkhani za chuma
CCAP 1) Pemphererani kagwiritsidwe ntchito
Blantyre kabwino ka chuma cha Synod.
Synod 2) Kumbukiraninso abusa opuma amene
Day 11 Deuteronomo
ambiri mwa iwo akuvutika.
(12/01/2024) 10:14
3) Mulungu avumbulutse mwa atsogoleri
athu njira zina zopezera chuma.
4) Akhristu akhulupirike pakupereka za
malumbiro pofuna kuthandiza Synod.
* Udindo wa mpingo
1) Mpingo wathu udzitha kuyankhula
motsutsana ndi uchimo m’dziko muno.
2) Mpingo udzitha kuyankhulira iwo amene
Day 12
ali oponderezedwa komanso ovutika. Miyambo 31:8-9
(13/01/2024)
3) Mpingo usakhale chete pa malamulo
otsutsana ndi mau a Mulungu m’dzikoli.
4) Mpingo usatsamire ku chipani cha ndale
koma uyime pa chilungamo.
Mlombwa CCAP – Evangelism Department 2 of 4
* Dziko lathu ndilodala
1) Yamikani Mulungu chifukwa cha nthaka
yabwino.
2) Yamika Mulungu chifukwa cha nyengo
yabwino.
Day 13
3) Yamikani Mulungu chifukwa cha madzi Masalmo 107:1-3
(14/01/2024)
ochuluka omwe alipo m’dziko lathu.
4) Yamikani Mulungu chifukwa dziko lathu
ndi la mtendere, losadziwa nkhondo.
5) Yamikani Mulungu potipambanitsa ku
miliri ya mu 2023.
* Utsogoleri wa dziko
1) Pempherani kuti atsogoleri athu akhale
ndi mtima owopa Mulungu.
2) Atsogoleri athu atumikire mokhulupirika
Day 14
komanso moona mtima. 1 Timoteo 2:1-4
(15/01/2024)
3) Atsogoze moyo wa aMalawi onse osati
kulingalira zawo zokha.
4) Atsogoleri azindikire kuti Mulungu
Dziko la anawaika pa udindo ndi cholinga.
Malawi * Chuma cha dziko lathu
1) Pempherani kuti mitengo ya zinthu
ikhazikike. Zinthu zikakwera kwambiri
mtengo zimabweretsa mavuto kwa anthu.
2) Mulungu atithandize kuti tikolole
Day 15
zokwanira popeza chuma chathu Afilipi 4:19-20
(16/01/2024)
chimadalira za ku munda.
3) Tikhale ndi chakudya chokwanira kwa
m’Malawi wina aliyense.
4) Pemphererani kukhazikika kwa
mphamvu ya ndalama yathu.
* Atsogoleri a ndale
1) Atsogoleri andale ayike mtima wao
pakutukula a Malawi.
2) Mu zochita zawo alingalire kwambiri
Day 16
munthu osauka wa kumudzi. Ahebri 13:16
(17/01/2024)
3) Atsogoleriwa asachite zinthu ndi mtima
wa njiru, koma atsogoze chikondi.
4) Apewe komanso alimbane ndi katangale
amene ali mdani wa chitukuko.
1) Pemphererani abale ndi anzanu amene
sanatembenukebe mtima mpaka lero.
Abale ndi Day 17 2) Pemphererani abale ndi anzanu amene
Aroma 1:9
anzathu (18/01/2024) samakonda kupemphera.
3) Pemphererani abale ndi anzanu amene
amakonda kujomba-jomba ku tchalitchi.

Mlombwa CCAP – Evangelism Department 3 of 4


4) Pemphererani abale ndi anzanu amene
akusowa ntchito kapena chochita.
5) Pempherani motsutsana ndi
matemberero a kumtundu.
1) Pemphererani ana a masiye onse amene
akuvutika kupeza thandizo pa moyo wawo.
2) Pemphererani azimayi amasiye onse
Amasiye amene akuvutika kusamalira banja lawo.
Day 18
ndi 3) Pemphererani okalamba onse amene Masalmo 82:3-4
(19/01/2024)
okalamba nawonso akuvutika kupeza chakudya
ngakhalenso nyumba yogonamo.
4) Lingalirani zotengapo gawo pa
kusamalira anthu ngati amenewa.
1) Pemphererani abale, anzanu, komanso
ena onse amene akudwala.
2) Pemphani Mulungu alimbikitse ma
Odwala dokotala ndi ena onse amene akuthandizira
Day 19
ndi kusamalira odwala. Aroma 12:15
(20/01/2024)
oferedwa 3) Kumbukiraninso iwo amene aferedwa
kuti Mulungu mwini awatonthoze.
4) Mulungu apukute misozi yawo
ndikuwapatsa chiyembekezo m’moyo wao.
1) Lengezani madalitso pa banja lanu.
Kulengeza 2) Lengezani madalitso pa business yanu.
madalitso Day 20 3) Lengezani madalitso pa ntchito yanu.
Miyambo 3:5
pa moyo (21/01/2024) 4) Lengezani madalitso pa sukulu yanu.
wanu 5) Lankhulani madalitso pa ma plan anu.
6) Nenerani madalitso pa mpingo wanu.
1) Yamikani Mulungu pakuti
ndiwokhulupirika.
2) Yamikani Mulungu pakuti wamva
kupempha ndi kulira kwanu.
3) Yamikani Mulungu pakuti wayankha
Kuthokoza Day 21 mapemphero anu.
Marko 11:24
Mulungu (22/01/2024) 4) Yamikani Mulungu pakuti nthawi zonse
ali nafe, ndipo samatisiya tokha.
5) Yamikani Mulungu chifukwa watikonzera
njira mu 2024.
6) Yamikani Mulungu chifukwa cha
madalitso komanso chipambano chake.

Mlombwa CCAP – Evangelism Department 4 of 4

You might also like